8 Mwana wa Palu anali Eliabu, 9 ndipo ana a Eliabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali gulu la akuluakulu aja amene anawukira Mose ndi Aaroni ndipo analinso mʼgulu la otsatira Kora pamene anawukira Yehova. 10 Nthaka inangʼambika ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lawo linafa pamene moto unapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo. 11 Koma ana a Kora sanafe nawo.
12 Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi:
kuchokera mwa Nemueli, fuko la Anemuele;
kuchokera mwa Yamini, fuko la Ayamini;
kuchokera mwa Yakini fuko la Ayakini;
13 kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera;
kuchokera mwa Sauli, fuko la Asauli.
14 Awa anali mafuko a Simeoni. Iwowa analipo amuna 22,200.
15 Zidzukulu za Gadi mwa mafuko awo ndi izi:
kuchokera mwa Zefoni, fuko la Azefoni;
kuchokera mwa Hagi, fuko la Ahagi;
kuchokera mwa Suni, fuko la Asuni;
16 kuchokera mwa Ozini, fuko la Aozini;
kuchokera mwa Eri, fuko la Aeri;
17 kuchokera mwa Arodi, fuko la Aarodi;
kuchokera mwa Arieli, fuko la a Areli.
18 Awa ndiwo anali mafuko a Gadi. Onse amene anawerengedwa analipo 40,500.
19 Eri ndi Onani anali ana aamuna a Yuda, koma anafera mu Kanaani.
20 Zidzukulu za Yuda monga mwa mafuko awo zinali izi:
51 Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730.
52 Yehova anawuza Mose kuti, 53 “Uwagawire dziko anthu awa kuti likhale cholowa chawo molingana ndi chiwerengero cha mayina awo. 54 Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa. 55 Dzikolo uligawe pochita maere. Alandire cholowa chawocho potsata mayina a mafuko a makolo awo. 56 Cholowa chawo uchigawe pakati pa fuko lalikulu ndi lalingʼono mwa maere.”
57 Alevi omwe anawerengedwa monga mwa mafuko awo ndi awa:
kuchokera mwa Geresoni, fuko la Ageresoni;
kuchokera mwa Kohati, fuko la Akohati;
kuchokera mwa Merari, fuko la Amerari.
58 Awanso anali mabanja a Alevi:
banja la Alibini,
banja la Ahebroni,
banja la Amali,
banja la Amusi, fuko la Kora
banja la Akohati,
(Kohati anali abambo a Amramu. 59 Dzina la mkazi wa Amramu linali Yokobedi, mdzukulu wa Levi, yemwe anabadwa mwa Alevi mu Igupto. Yokobedi anaberekera Amramu Aaroni, Mose ndi Miriamu mlongo wawo. 60 Aaroni anali abambo a Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. 61 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo).
62 Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo.
63 Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko. 64 Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai; 65 Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.