1 Pa tsiku la 24 la mwezi womwewo, Aisraeli anasonkhana pamodzi ndi kusala chakudya, kuvala ziguduli ndi kudzithira dothi pa mutu. 2 Aisraeliwa anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anayimirira nayamba kuwulula machimo awo ndi zolakwa za makolo awo. 3 Anthuwo anayimirira pomwepo, ndipo anamva mawu a mʼbuku la malamulo a Yehova akuwerengedwa kwa maora enanso atatu ndipo anakhala maora ena atatu akuwulula machimo awo ndi kupembedza Yehova Mulungu wawo. 4 Pa makwerero okhalapo alevi anayimirirapo anthu awa: Yesuwa, Bani, Kadimieli, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani ndi Kenani. Iwowa ankapemphera mokweza mawu kwa Yehova Mulungu wawo. 5 Ndipo Alevi awa: Yesuwa, Kadimieli, Bani, Hasabaneya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya anati: “Imirirani ndipo mutamande Yehova Mulungu wanu, amene ndi wamuyaya.”
“Litamandike dzina lake laulemerero limene liposa madalitso ndi matamando onse. 6 Inu nokha ndiye Yehova. Munalenga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, zolengedwa zonse zimene zili mʼmenemo. Munalenga dziko ndi zonse zokhalamo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo. Zonse mumazisunga ndi moyo ndipo zonse za kumwamba zimakupembedzani.
7 “Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumutulutsa mʼdziko la Uri wa ku Kaldeya ndi kumutcha dzina lake Abrahamu. 8 Inu munaona kuti mtima wake unali wokhulupirika kwa inu, ndipo munapangana naye pangano lakuti mudzapereka kwa zidzukulu zake dziko la Akanaani Ahiti, Aamori, Aperezi, Ayebusi ndi Agirigasi. Inu mwasunga lonjezo lanu chifukwa ndinu wolungama.
9 “Munaona kuzunzika kwa makolo athu ku Igupto. Munamva kufuwula kwawo pa Nyanja Yofiira. 10 Inu munachita zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa kutsutsana ndi Farao, pamaso pa Farao, nduna zake ndi anthu onse a mʼdziko lake, pakuti Inu munadziwa kuti anazunza makolo athu. Inu munadzipangira nokha dzina, monga zilili mpaka lero lino. 11 Inu munagawa nyanja anthu anu akupenya, kotero kuti anadutsa powuma, koma munamiza mʼmadzi akuya anthu amene ankawalondola monga mmene uchitira mwala mʼmadzi ozama. 12 Masana munkawunikira ndi chipilala cha mtambo ndipo usiku munkawunikira ndi chipilala cha moto njira yonse imene ankayendamo.
13 “Munatsika pa Phiri la Sinai, ndipo munawayankhula kuchokera kumwamba. Munawapatsa malangizo olungama, ziphunzitso zoona ndiponso malamulo abwino. 14 Inu munawadziwitsa kuti tsiku lanu la Sabata ndi loyera ndipo munawapatsa malamulo ndi ziphunzitso. 15 Pamene anali ndi njala munawapatsa buledi wochokera kumwamba. Pamene anali ndi ludzu munawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe. Munawawuza kuti apite kukalanda dziko limene munalonjeza kuti mudzawapatsa.”
16 “Koma makolo athu anadzikuza ndi kuwumitsa khosi, ndipo iwo sanamvere malamulo anu. 17 Anakana kumvera ndipo sanakumbukire zodabwitsa zimene munachita pakati pawo. Koma iwo anawumitsa khosi, nakuwukirani podzisankhira okha mtsogoleri kuti awatsogolere kubwerera ku ukapolo ku dziko la Igupto. Koma ndinu Mulungu wokhululukira, wokoma mtima ndi wachifundo wosapsa mtima msanga ndi wachikondi chachikulu chosasinthika. Choncho Inu simunawasiye. 18 Ngakhale pamene iwo anadziwumbira fano la mwana wangʼombe ndi kuti, ‘Uyu ndi mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto,’ kapena pamene anachita chipongwe choopsa.
19 “Koma Inu ndi chifundo chanu chachikulu, simunawasiye mʼchipululu. Chipilala cha mtambo sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo masana ndipo chipilala cha moto sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo usiku. 20 Inu munawapatsa mzimu wanu wabwino kuti uwalangize. Inu simunawamane chakudya cha mana chija, ndipo munawapatsa madzi akumwa. 21 Munawasunga zaka makumi anayi mʼchipululu ndipo sanasowe kanthu kalikonse. Zovala zawo sizinathe kapena mapazi awo kutupa.”
22 “Inu munawapatsa mafumu ndi mayiko mʼmanja mwawo. Munawagawiranso mayiko achilendo akutali kwambiri. Munabwera nawo mʼdziko la Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani kuti alowemo nʼkulitenga kukhala lawo. 23 Munachulukitsa ana awo aamuna ngati nyenyezi za mlengalenga. Ndipo munawabweretsa mʼdziko limene munawuza makolo awo kuti alilowe ndi kulitenga. 24 Choncho zidzukulu zawo zinapita ndi kukalandira dzikolo. Inu munagonjetsa pamaso pawo, Akanaani amene amakhala mʼdzikolo. Inde munapereka mʼmanja mwawo mafumu awo pamodzi ndi anthu a mʼdzikomo kuti achite nawo monga angafunire. 25 Iwo analanda mizinda yotetezedwa ndi dziko lachonde. Anatenganso nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino, zitsime zokumbidwa kale, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndi mitengo yambiri ya zipatso. Ndipo anadya nakhuta ndipo anali athanzi. Choncho ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu wopambana.