1 Patapita masiku pangʼono, Yesu atalowanso mu Kaperenawo, zinamveka kuti wabwera ali mʼnyumba. 2 Choncho anthu ambiri anasonkhana kotero kuti panalibenso malo, ngakhale ndi pa khomo pomwe, ndipo Iye anawalalikira mawu. 3 Amuna anayi anabwera, atanyamula munthu wofa ziwalo. 4 Popeza sakanatha kufika naye kwa Yesu chifukwa cha gulu la anthu, anasasula denga chapamwamba pamene panali Yesu, ndipo atabowoleza, anatsitsa mphasa yomwe munthu wofa ziwaloyo anagonapo. 5 Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati kwa wofa ziwaloyo,
6 Ndipo ena mwa aphunzitsi amalamulo anakhala pansi pomwepo, namaganiza mʼmitima mwawo kuti, 7 “Nʼchifukwa chiyani munthuyu ayankhula chotere? Iye akuchitira mwano Mulungu! Ndani angakhululukire munthu machimo kupatula Mulungu yekha?”
8 Nthawi yomweyo Yesu anadziwa mu mzimu wake kuti izi ndi zimene ankaganiza mʼmitima yawo, ndipo anawawuza kuti,
13 Yesu anatulukanso napita kumbali ya nyanja. Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye, ndipo anayamba kuliphunzitsa. 14 Pamene ankayendabe, anaona Levi mwana wa Alufeyo atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anamuwuza kuti,
15 Yesu atakalandira chakudya ku nyumba kwa Levi, amisonkho ambiri ndi “ochimwa” ankadya naye pamodzi ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri amene anamutsatira. 16 Pamene aphunzitsi amalamulo a Afarisi anamuona akudya ndi “ochimwa” ndi amisonkho, anafunsa ophunzira ake kuti, “Chifukwa chiyani amadya ndi olandira msonkho ndi ochimwa?”
17 Yesu atamva zimenezi, anawawuza kuti,
18 Ndipo ophunzira a Yohane ndi a Afarisi amasala kudya. Anthu ena anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Zitheka bwanji kuti ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma anu satero?”
19 Yesu anayankha nati,
21
23 Tsiku lina la Sabata, Yesu amadutsa pakati pa minda ya tirigu, ndipo ophunzira ake amayenda naye limodzi, nayamba kubudula ngala za tiriguyo. 24 Afarisi anati kwa Iye, “Taonani, chifukwa chiyani akuchita chosaloledwa ndi lamulo pa Sabata?”
25 Iye anayankha kuti,
27 Pamenepo anawawuza kuti,