1 Yesu atamaliza kuyankhula zonsezi, anati kwa ophunzira ake, 2
3 Pamenepo akulu a ansembe ndi akuluakulu anasonkhana ku nyumba ya mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa, 4 ndipo anapangana kuti amugwire Yesu mobisa ndi kumupha. 5 Ndipo anati, “Osati nthawi yaphwando chifukwa pangabuke chipolowe pakati pa anthu.”
6 Yesu ali ku Betaniya mʼnyumba Simoni Wakhate, 7 mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo.
8 Ophunzira ataona izi anayipidwa nafunsa kuti, “Chifukwa chiyani akuwononga chotere? 9 Mafuta amenewa akanatha kugulitsidwa pa mtengo waukulu, ndipo ndalama zake zikanaperekedwa kwa osauka.”
10 Yesu podziwa izi anawawuza kuti,
14 Pamenepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo wotchedwa Yudasi Isikarioti anapita kwa akulu a ansembe 15 nafunsa kuti, “Kodi mundipatsa chiyani ngati nditamupereka Iye kwa inu?” Pamenepo anamuwerengera ndalama zokwanira masiliva makumi atatu. 16 Kuyambira pamenepo Yudasi anafunafuna nthawi yabwino yoti amupereke Yesu.
17 Pa tsiku loyamba laphwando la buledi wopanda yisiti, ophunzira anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonze kuti malo odyera Paska?”
18 Iye anayankha kuti,
20 Kutada, Yesu ndi ophunzira ake khumi ndi awiriwo anakhala pa tebulo nʼkumadya. 21 Akudya, Iye anati,
22 Iwo anamva chisoni kwambiri ndipo anayamba kuyankhulana naye mmodzimmodzi nati, “Kodi nʼkukhala ine Ambuye?”
23 Yesu anayankha nati,
25 Ndipo Yudasi amene anamupereka Iye anati, “Monga nʼkukhala ine Aphunzitsi?”
26 Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti,
27 Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo nati,
30 Atayimba nyimbo, anatuluka kupita ku phiri la Olivi.
31 Pamenepo Yesu anawawuza kuti,
33 Petro anayankha nati, “Ngakhale onsewa atakuthawani, ine ndekha ayi.”
34 Yesu anayankha nati,
35 Koma Petro ananenetsa nati, “Ngakhale kutakhala kufa nanu pamodzi, sindidzakukanani.” Ndipo ophunzira onse ananena chimodzimodzi.
36 Kenaka Yesu anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo anawawuza kuti,
39 Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi chafufumimba napemphera kuti,
40 Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nawapeza ali mtulo. Iye anafunsa Petro kuti,
42 Anachokanso nakapemphera kachiwiri kuti,
43 Atabweranso anawapeza ali mtulo chifukwa zikope zawo zinalemedwa ndi tulo. 44 Choncho anawasiya napitanso kukapemphera kachitatu nanenanso chimodzimodzi.
45 Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nati kwa iwo,
47 Akuyankhula choncho, Yudasi mmodzi mwa khumi ndi awiriwo anafika. Pamodzi ndi iye panali gulu lalikulu la anthu ali ndi mikondo ndi zibonga otumidwa ndi akulu a ansembe ndi akuluakulu. 48 Womuperekayo anawawuziratu chizindikiro anthuwo kuti, “Amene ndidzapsompsona ndi iyeyo; mugwireni.” 49 Pamenepo Yudasi anapita kwa Yesu nati, “Moni, Aphunzitsi!” Ndipo anapsompsona Iye.
50 Yesu anayankha kuti,
52 Yesu anati kwa iye,
55 Pa nthawi yomweyo Yesu anati kwa gululo,
57 Iwo amene anamugwira Yesu anamutengera kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anasonkhana. 58 Koma Petro anamutsatira Iye patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Analowa nakhala pansi pamodzi ndi alonda kuti aone zotsatira.
59 Akulu a ansembe ndi akulu olamulira Ayuda amafunafuna umboni wonama wofuna kuphera Yesu. 60 Koma sanathe kupeza uliwonse, angakhale kuti mboni zambiri zabodza zinapezeka.
62 Pamenepo mkulu wa ansembe anayimirira nati kwa Yesu, “Kodi suyankha? Kodi umboni umenewu ndi otani umene anthu awa akupereka kukutsutsa Iwe?” 63 Koma Yesu anakhalabe chete.
64 Yesu anayankha nati,
65 Pamenepo mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zake nati, “Wanyoza Mulungu! Tifuniranji mboni zina? Taonani, tsopano mwamva mwano wake. 66 Mukuganiza bwanji?”
67 Kenaka anamulavulira kumaso namumenya ndi zibakera. Ena anamumenya makofi. 68 Ndipo anati, “Tanenera kwa ife, Khristu. Wakumenya ndani?”
69 Tsopano Petro anakhala ku bwalo la nyumbayo, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye nati, “Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.”
70 Koma iye anakana pamaso pawo nati, “Sindikudziwa chimene ukunena.”
71 Kenaka anachoka kupita ku khomo la mpanda, kumene mtsikana wina anamuonanso nawuza anthu nati, “Munthu uyu anali ndi Yesu wa ku Nazareti.”
72 Iye anakananso molumbira kuti, “Sindimudziwa munthuyu!”
73 Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pamenepo anapita kwa Petro nati, “Zoonadi, ndiwe mmodzi wa iwo, popeza mayankhulidwe ako akukuwulula.”
74 Pamenepo anayamba kudzitemberera ndipo analumbira kwa iwo nati, “Sindimudziwa munthu ameneyo!”