1 Pa tsiku loyamba la Sabata, mmamawa kwambiri, amayi anatenga zonunkhira napita ku manda. 2 Anaona mwala wa pa manda utagubuduzika 3 ndipo atalowamo sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu. 4 Pamene iwo ankadabwa za zimenezi, mwadzidzidzi, amuna awiri ovala zovala zonyezimira kwambiri anayimirira pambali pawo. 5 Ndi mantha, amayiwo anaweramitsa nkhope zawo pansi, koma amunawo anawawuza kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufuna wamoyo pakati pa akufa? 6 Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya: 7
9 Atabwerera kuchokera ku mandako, anafotokoza zinthu zonse kwa khumi ndi mmodziwo ndi kwa ena onse. 10 Amayi anali Mariya Magadalena, Yohana, Mariya amayi a Yakobo, ndi ena anali nawo amene anawuza atumwi. 11 Koma iwo sanawakhulupirire amayiwa, chifukwa mawu awo amaoneka kwa iwo ngati opanda nzeru. 12 Komabe Petro anayimirira ndi kuthamangira ku manda. Atasuzumira, anaona nsalu zimene anamukulungira zija zili pa zokha, ndipo iye anachoka, akudabwa ndi zimene zinachitikazo.
13 Ndipo tsiku lomwelo, awiri a iwo ankapita ku mudzi wotchedwa Emau, pafupifupi makilomita khumi ndi imodzi kuchokera ku Yerusalemu. 14 Iwo ankayankhulana za zonse zimene zinachitikazo. 15 Pamenepo Yesu mwini wake anabwera ndi kuyenda nawo pamodzi; 16 koma iwo sanamuzindikire.
17 Iye anawafunsa kuti,
19 Iye anafunsa kuti,
25 Iye anawawuza kuti,
28 Atayandikira mudzi omwe amapitako, Yesu anachita ngati akupitirira. 29 Koma iwo anamupempha Iye kwambiri kuti, “Mukhale ndi ife, popeza kwatsala pangʼono kuda, ndipo dzuwa lili pafupi kulowa.” Ndipo Iye anapita kukakhala nawo.
30 Iye ali pa tebulo pamodzi nawo, anatenga buledi ndipo anayamika, nanyema nayamba kuwagawira. 31 Kenaka maso awo anatsekuka ndipo anamuzindikira Iye, ndipo anachoka pakati pawo. 32 Iwo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi mitima yathu sinali kutentha mʼkati mwathu pamene Iye ankayankhulana nafe pa njira ndi mmene anatitsekulira malemba?”
33 Nthawi yomweyo iwo anayimirira ndi kubwerera ku Yerusalemu. Iwo anapeza khumi ndi mmodziwo ndi ena anali nawo nasonkhana pamodzi 34 ndipo anati, “Ndi zoonadi! Ambuye auka ndipo anaonekera kwa Simoni.” 35 Kenaka awiriwo anawawuza zimene zinachitika pa njira, ndi mmene iwo anamudziwira Yesu, Iye atanyema buledi.
36 Akufotokoza zimenezi, Yesu mwini wake anayimirira pakati pawo ndipo anati,
37 Koma chifukwa choti anathedwa nzeru ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzukwa. 38 Iye anawafunsa kuti,
40 Iye atanena izi anawaonetsa manja ake ndi mapazi ake. 41 Ndipo pamene iwo samakhulupirirabe, chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, Iye anawafunsa kuti,
44 Iye anawawuza kuti,
45 Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba. 46 Iye anawawuza kuti,
50 Iye atawatengera kunja kwa mzindawo mpaka ku Betaniya, anakweza manja ake ndi kuwadalitsa. 51 Iye akuwadalitsa, anawasiya ndipo anatengedwa kupita kumwamba. 52 Pamenepo anamulambira Iye ndipo anabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. 53 Ndipo iwo anakhalabe ku Nyumba ya Mulungu, akulemekeza Mulungu.