1 Popeza lonjezo lakuti tidzalowe mu mpumulo umene anatilonjeza lilipobe, tiyeni tisamale kuti pasakhale wina aliyense mwa inu wodzalephera kulowamo. 2 Pakuti Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa ife, monganso iwo aja; koma iwo sanapindule nawo uthengawo chifukwa anangomva koma osakhulupirira. 3 Tsono ife amene takhulupirira talowa mu mpumulo, monga momwe Mulungu akunenera kuti,
6 Popeza kwatsalabe kuti ena adzalowe mu mpumulowo, koma aja anayamba kumva Uthenga Wabwino sanalowe chifukwa cha kusamvera kwawo. 7 Nʼchifukwa chake Mulungu anayikanso tsiku lina limene analitcha “Lero.” Patapita nthawi yayitali Iye anayankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide, monga ndinanena kale kuti,
12 Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima. 13 Palibe kanthu kobisika pamaso pa Mulungu. Zinthu zonse zili poyera ndi zovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.
14 Popeza kuti tili ndi Mkulu wa ansembe wopambana, amene analowa kale kumwamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tiyeni tigwiritsitse chikhulupiriro chathu chimene timavomereza. 15 Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe. 16 Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.
<- AHEBRI 3AHEBRI 5 ->