15 Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu,
linga lolimba la Igupto,
ndi kuwononga gulu lankhondo la Thebesi.
16 Ndidzatentha ndi moto dziko la Igupto;
Peluziumu adzazunzika ndi ululu.
Malinga a Thebesi adzagumuka,
ndipo mzindawo udzasefukira ndi madzi.
17 Anyamata a ku Oni ndi ku Pibeseti
adzaphedwa ndi lupanga
ndipo okhala mʼmizinda yake adzatengedwa ukapolo.
18 Ku Tehafinehezi kudzakhala mdima
pamene ndidzathyola goli la Igupto;
motero kunyada kwake kudzatha.
Iye adzaphimbidwa ndi mitambo yakuda,
ndipo okhala mʼmizinda yake adzapita ku ukapolo.
19 Kotero ndidzalanga dziko la Igupto,
ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
Farao Watha Mphamvu
20 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi woyamba wa chaka chakhumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: 21 “Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Igupto. Taona, silinamangidwe kuti lipole, ngakhale kulilimbitsa ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga. 22 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake. 23 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. 24 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo. 25 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto. 26 Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu, ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”