1 Choncho mfumu ndi Hamani anabwera kudzadya phwando la mfumukazi Estere. 2 Pa tsiku lachiwiri akumwa vinyo, mfumu inafunsanso kuti, “Kodi iwe mfumukazi Estere, chimene ufuna kupempha nʼchiyani? Chimene uti upemphe ndidzakupatsa. Choncho ukufuna chiyani? Ngakhale utafuna theka la ufumu ndidzakupatsa.”
3 Kenaka mfumukazi Estere anayankha kuti, “Ngati mwandikomera mtima, inu mfumu, ndipo ngati chingakukomereni mfumu, pempho ndi chokhumba changa ndi ichi, mulole kuti ine ndi abale anga tisungidwe tonse ndi moyo. 4 Popeza ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa kuti atiwononge, atiphe ndi kutifafaniziratu. Akanangotigulitsa kokha tikanakhala chete, chifukwa chimene mdani wathuyo akanakupatsani mfumu sibwenzi mutasowa nacho mtendere.”
5 Mfumu Ahasiwero anamufunsa mfumukazi Estere, “Kodi iyeyu ndi ndani ndipo ali kuti amene saopa kuchita chinthu chotere?”
6 Estere anati, “Wotizunza ndiponso mdani wathu! Munthu woyipayo ndi Hamani.”
8 Mfumu itabwerera kuchokera ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu uja ndi kulowanso mʼchipinda chaphwando, anapeza Hamani atagona chafufumimba pa mpando wa khutagone pomwe Estere anakhalapo.